Genesis 38:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi yochira, mmodzi mwa anawo adatulutsa dzanja. Mzamba adaligwira, nalimanga ndi chingwe chofiira nati, “Ameneyu ndiye woyamba kubadwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali pamene anabala kuti mmodzi anatulutsa dzanja; ndipo namwino anatenga chingwe chofiira namanga pa dzanja lake, kuti, Uyu anayamba kubadwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ankabereka, mmodzi wa iwo anatulutsa dzanja lake. Choncho mzamba anatenga kawulusi kofiira nakamangirira pa mkono pa mwanayo nati, “Uyu ndiye anayamba kubadwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali pamene anabala kuti mmodzi anaturutsa dzanja; ndipo namwino anatenga cingwe cofiira namanga pa dzanja lace, kuti, Uyu anayamba kubadwa.