Genesis 38:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mwanayo adalibweza dzanja lake, mwakuti mbale wake ndiye adayambira kubadwa. Tsono mzamba uja adati, “Uchita kudziphothyolera wekha chotere!” Motero mwanayo adatchedwa Perezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali pamene iye anabweza dzanja lake, kuti, taona, mbale wake anabadwa, ndipo namwino anati, Wadziposolera wekha bwanji? Chifukwa chake dzina lake linatchedwa Perezi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene anabweza mkonowo, mʼbale wake anabadwa ndipo mzamba anati, “Wachita kudziphotcholera wekha njira chonchi!” Ndipo anamutcha Perezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali pamene iye ana bweza dzanja lace, kuti, taona, mbale wace anabadwa, ndipo namwino anati, Wadziposolera wekha bwanji? cifukwa cace dzina lace linachedwa Pereze.