Genesis 39:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aismaele aja adapita naye Yosefe ku Ejipito kumene Potifara Mwejipito, nduna ya Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda kunyumba ya mfumu, adamgula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Ejipito; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, Mwejipito, anamgula iye m'manja mwa Aismaele amene anatsika naye kunka kumeneko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano Yosefe anatengedwa kupita ku Igupto. Potifara Mwigupto amene anali mmodzi wa akuluakulu a Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa Farao, anagula Yosefe kwa Aismaeli amene anapita naye kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Aigupto; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, Maigupto, anamgula iye m'manja mwa Aismayeli amene anatsika naye kunka iumeneko.