Genesis 39:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkazi uja adamgwira mwinjiro Yosefeyo, namuuza kuti, “Ugone nane basi!” Koma iye adathaŵira pabwalo, kusiya mwinjiro uja uli m'manja mwa mkaziyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkazi anagwira iye chofunda chake, nati, Gona ndi ine; ndipo anasiya chofunda chake m'dzanja lake nathawa, natulukira kubwalo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkazi uja anamugwira mkanjo Yosefe nati, “Tiye ugone nane!” Koma Yosefe anasiya mkanjo wake mʼmanja mwa mkaziyo nathawira kunja kwa nyumba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkazi anagwira iye copfunda cace, nati, Gona ndi ine; ndipo anasiya copfunda cace m'dzanja lace nathawa, naturukira kubwalo.