Genesis 39:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
adaitana antchito am'nyumbamo, naŵauza kuti, “Mwaziwona izi? Mwamuna wanga adabwera ndi Muhebri uyu m'nyumba muno kudzatipunza ife. Iye anakaloŵa kuchipinda kwanga nandinyenga kuti ndigone naye. Koma ine ndinakuŵa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
anaitana amuna a m'nyumba yake, nanena ndi iwo kuti, Taonani, walowetsa kwa ife Muhebri kuti atiseke ife, analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinafuula ndi mau akulu:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
iye anayitana antchito ake a mʼnyumba nati, “Taonani mwamuna wanga anabwera ndi Mhebri uyu mʼnyumba muno kuti adzagone nane. Iyeyu analowa ku chipinda kwanga kuti adzagone nane ndipo ine ndinakuwa kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
anaitana amuna a m'nyumba yace, nanena ndi iwo kuti, Taonani, walowetsa kwa ife Mhebri kuti atiseke ife, analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinapfuula ndi mau akuru: