Genesis 39:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbuyake wa Yosefe adapsa mtima koopsa atamva mau a mkazi wake onena kuti, “Inde, izi ndi zimene wandichita kapolo wanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali pamene mbuyake anamva mau a mkazi wake, amene ananena kwa iye, kuti, Choterochi anandichitira ine kapolo wako; kuti iye anapsa mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbuye wake wa Yosefe atamva nkhani imene mkazi wake anamuwuza kuti, “Ndi zimene anandichitira wantchito wanu,” anapsa mtima kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali pamene mbuyace anamva mau a mkazi wace, amene ananena kwa iye, kuti, Coteroci anandicitira ine kapolo wako; kuti iye anapsya mtima.