Genesis 39:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zonse zinali m'manja mwa Yosefe, ndipo wosunga ndendeyo sankayang'aniranso kanthu kena kalikonse, chifukwa Chauta anali naye Yosefe ndipo ankamukhozetsa pa zonse zimene ankachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Woyang'anira m'kaidi sanayang'anire kanthu kalikonse kamene kanali m'manja a Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi iye; ndipo zimene anazichita, Yehova anazipindulitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Woyangʼanira ndende uja sankayangʼaniranso china chilichonse chimene chinali mu ulamuliro wa Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi Yosefe. Ndipo Yehova anaonetsetsa kuti chilichonse chimene Yosefe ankachita chimuyendere bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Woyang'anira m'kaidi sanayang'anira kanthu kali konse kamene kanali m'manja a Yosefe, cifukwa Yehova anali ndi iye; ndipo zimene anazicita, Yehova anazipindulitsa.