Genesis 39:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuyambira nthaŵi imene Yosefe adayamba kusamalira zonse za m'nyumba ya Potifarayo, Chauta adadalitsa zonse za kunyumba kwa Mwejipitoyo, ngakhale za kuminda kwake, chifukwa cha Yosefeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali chiyambire anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, ndi pa zake zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwejipito chifukwa cha Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zake zonse, m'nyumba ndi m'munda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera pa nthawi imene anamuyika kukhala woyangʼanira wa nyumbayo ndi zonse za mʼnyumbamo, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwiguptoyo chifukwa cha Yosefe. Madalitso a Yehova anali pa chilichonse chimene Potifara anali nacho, za mʼnyumba komanso za ku munda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali ciyambire anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yace, ndi pa zace zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya M-aigupto cifukwa ca Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zace zonse, m'nyumba ndi m'munda.