Genesis 39:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Potifara adaika m'manja mwa Yosefe zake zonse, kotero kuti sankalabadiranso kanthu kalikonse, koma chakudya chokha chimene ankadya. Yosefe anali wa maonekedwe abwino ndi wokongola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anasiya zake zonse m'manja a Yosefe: osadziwa chomwe anali nacho, koma chakudya chimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anasiyira mʼmanja mwa Yosefe chilichonse chomwe anali nacho, kotero kuti samadandaula ndi chilichonse kupatula chakudya chimene ankadya. Tsopano Yosefe anali wa thupi labwino ndi wokongola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anasiya zace zonse m'manja a Yosefe; osadziwa comwe anali naco, koma cakudya cimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola.