Genesis 39:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo ulamuliro wa zonse za m'nyumba muno uli m'manja mwanga, osati m'manja mwake. Sadandimane kanthu kalikonse kupatula inu nokha, pakuti ndinu mkazi wake. Tsono kungatheke bwanji kuti ine ndichite chinthu choipitsitsa choterechi, ndi kuchimwira Mulungu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero kuti palibe wina wamkulu kuposa ine mʼnyumba muno. Ndipo palibe chilichonse chimene mbuye wanga sanachipereke kwa ine kupatula inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Tsono ndingachite bwanji choyipa choterechi ndi kuchimwira Mulungu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mulibe wina m'nyumba wamkuru ndine; ndipo sanandikaniza ine kanthu, koma iwe, cifukwa kuti uli mkazi wace: nanga ndikacita coipa cacikuru ici bwanji ndi kucimwira Mulungu?