Genesis 4:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamu adakhala ndi mkazi wake Heva ndipo mkaziyo adatenga pathupi. Tsono adabala mwana wamwamuna, ndipo adati, “Ndalandira mwana wamwamuna mwa chithandizo cha Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Kaini.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, “Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wace Hava: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.