Genesis 4:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta adamuyankha kuti, “Iyai, aliyense wopha iwe Kaini adzalangidwa, ndipo Ineyo ndidzamulipsira kasanunkaŵiri.” Motero Chauta adaika chizindikiro pa Kaini kuchenjeza aliyense kuti asamuphe Kainiyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa iye, Chifukwa chake aliyense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika chizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe aliyense akampeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova anamuwuza kuti, “Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa iye, Cifukwa cace ali yense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika icizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe ali yense akampeza.