Genesis 4:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kaini adakhala ndi mkazi wake, mkaziyo adatenga pathupi, nabala mwana dzina lake Enoki. Tsono Kaini adamanga mzinda, nautcha dzina la mwana wake Enoki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wake; ndipo anatenga pakati, nabala Enoki: ndipo anamanga mudzi, nautcha dzina lake la mudziwo monga dzina la mwana wake, Enoki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kaini anagona malo amodzi ndi mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Enoki. Kaini nthawi imeneyo nʼkuti akumanga mzinda ndipo anawutcha dzina la mwana wake Enoki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wace; ndipo anatenga pakati, nabala Enoke: ndipo anamanga mudzi, naucha dzina lace la mudziwo monga dzina la mwana wace, Enoke.