Genesis 4:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Lameki adauza akazi akewo kuti, “Iwe Ada ndi iwe Zila, mverani mau anga. Tcherani khutu mumve, inu akazi anga. Ine ndapha munthu chifukwa anandipweteka. Ndamuphadi mnyamatayo amene anandimenya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lameki ndipo anati kwa akazi ake, Tamvani mau anga, Ada ndi Zila; inu akazi a Lameki, mverani kunena kwanga: Ndapha munthu wakundilasa ine, ndapha mnyamata wakundipweteka ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lameki anawuza akazi akewo kuti, “Ada ndi Zila, ndimvereni; inu akazi anga imvani mawu anga. Ine ndinapha munthu chifukwa anandipweteka. Ndinapha mnyamatayo chifukwa anandimenya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lameke ndipo anati kwa akazi ace: Tamvani mau anga, Ada ndi Zila; Inu akazi a Lameke, mverani kunena kwanga: Ndapha munthu wakundilasa ine, Ndapha mnyamata wakundiphweteka ine,