Genesis 4:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamu adakhalanso ndi Heva mkazi wake, ndipo adatenga pathupi nabala mwana. Tsono Hevayo adati, “Mulungu wandipatsa mwana woloŵa m'malo mwa Abele uja amene adaphedwa ndi Kaini.” Mwanayo adamutcha Seti.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti: Chifukwa, nati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu ina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adamu anagonanso malo amodzi ndi mkazi wake, ndipo anabereka mwana wamwamuna namutcha Seti, kutanthauza kuti, “Mulungu wandipatsa mwana wina mʼmalo mwa Abele, popeza Kaini anamupha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wace; ndipo anabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Seti: Cifukwa, nati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu yina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha,