Genesis 4:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ukadachita zabwino, ndikadakondwera nawe. Koma chifukwa choti wachita zoipa, tchimo lakukhalirira pa khomo ngati chilombo cholusa. Likulakalaka kuti likugwire, koma iweyo uligonjetse tchimolo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ukacita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kucita zabwino, ucimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwace, ndipo iwe udzamlamulira iye.