Genesis 4:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Kaini adauza mng'ono wake Abele kuti, “Tiye tikayende.” Atangopita kwa okha, Kaini adaukira mng'ono wakeyo namupha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwake. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwake, namupha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, “Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwace. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwace, namupha,