Genesis 40:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inetu adachita chondiba, ndipo adabwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri. Tsono ngakhale kunoko, sindidachite kanthu kalikonse koti anditsekere nako m'ndende.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m'dzenjemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popezatu ine anangochita mondiba kubwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri, ndipo ngakhale kunoko, ine sindinalakwe kali konse kuti ndizipezeka mʼdzenje muno.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinacite kanthu kakundiikira ine m'dzeniemu.