Genesis 40:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wophika buledi uja nayenso adaona kuti tanthauzo la malotowo linali labwino, adauza Yosefe kuti, “Inenso ndinalota nditasenza nsengwa zitatu za buledi pamutu pangapa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene wophika mkate anaona kuti kumasulira kwake kunali kwabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malichero atatu a mikate yoyera anali pamtu panga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkulu wa opanga buledi ataona kuti Yosefe wapereka tanthauzo labwino, anati kwa Yosefe, “Inenso ndinalota nditasenza nsengwa zitatu za buledi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene wophika mkate anaona kuti mmasuliro wace unali wabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malicero atatu a mikate yoyera anali pamtu panga;