Genesis 40:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usiku wina m'ndendemo, anthu aŵiri onse aja, woperekera vinyo uja ndi wophika buledi, adalota maloto. Aliyense mwa aŵiriwo adalota maloto ake a tanthauzo lakelake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analota maloto onse awiri, yense loto lake, usiku umodzi, yense monga mwa kumasulira kwa loto lake, wopereka chikho ndi wophika mkate wa mfumu ya Aejipito, amene anamangidwa m'kaidi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Usiku wina, aliyense wa anthu awiriwa, wopereka zakumwa pamodzi ndi wopanga buledi wa ku nyumba ya mfumu ya ku Igupto aja, amene ankasungidwa mʼndende, analota maloto. Malotowo anali ndi tanthauzo lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analota maloto onse awiri, yense lata lace, usiku umodzi, yense monga mwa kumasulira kwa loto lace, wopereka cikho ndi wophika mkate wa mfumu ya Aigupto, amene anamangidwa m'kaidi.