Genesis 40:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onsewo adayankha kuti, “Aŵirife tonse talota maloto usiku wapitawu, ndipo pano palibe ndi mmodzi yemwe wotha kutimasulira malotowo.” Apo Yosefe adaŵauza kuti, “Ndi Mulungu yekhatu amene amapatsa nzeru zomasulira maloto. Tandiwuzani maloto anuwo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tilibe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anayankha, “Tonse awiri talota maloto, koma palibe wotitanthauzira malotowo.” Pamenepo Yosefe anawawuza kuti, “Ndi Mulungu yekha amene amapereka matanthauzo a maloto. Uzeni ine maloto anu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tiribe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu.