Genesis 41:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'nyumba momwemo munali mnyamata wina Wachihebri, mtumiki wa mkulu wa alonda a m'ndende muja. Iyeyo adammasulira bwino aliyense mwa ife tanthauzo la maloto akewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali ndi ife mnyamata Muhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga loto lake anatimasulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono momwemo munali mnyamata wina Wachihebri, wantchito wa mkulu wa alonda. Ife tinamufotokozera maloto athu, ndipo anatitanthauzira malotowo. Munthu aliyense anamupatsa tanthauzo la loto lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali ndi ife mnyamata, Mhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga mwa loto lace anatimasulira.