Genesis 41:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo zidachitikadi monga momwe adaatimasulira. Ine ndidabwerera pa ntchito yanga, koma wophika buledi uja adampachika pa mtengo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudachitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampachika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo zinthu zinachitikadi monga mmene anatitanthauzira. Ine anandibwezera pa ntchito yanga ndipo winayo anapachikidwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudacitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampacika.