Genesis 41:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka padatulukanso ng'ombe zina zisanu ndi ziŵiri zoonda ndi za maonekedwe oipa kwambiri. Ng'ombe zimenezo zinali zoonda kwambiri kupambana ng'ombe zoonda zonse za m'dziko lonse la Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo taona, ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zina zinatuluka pambuyo pao zosauka ndi za maonekedwe oipa ndi zoonda, zoipa zotere sindinazione m'dziko la Ejipito;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka, ngʼombe zina zisanu ndi ziwiri zinatuluka. Izi zinali zosaoneka bwino ndiponso zowonda ndipo sindinaonepo ngʼombe zosaoneka bwino chonchi mʼdziko lonse la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo, taona, ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zina zinaturuka pambuyo pao zosauka ndi za maonekedwe oipa ndi zoonda, zoipa zotere sindinazione m'dziko la Aigupto;