Genesis 41:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zoonda zimene zidabwera pambuyo zija, ndiponso ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zopserera ndi mphepo yakuvuma zija, ndi zaka zisanu ndi ziŵiri za njala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinatuluka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngʼombe zisanu ndi ziwiri zowonda ndi zosaoneka bwino zimene zinatuluka pambuyozo ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zachabechabe, zowauka ndi mphepo ya kummawa zija ndi zaka zisanu ndi ziwiri za njala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinaturuka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopsyerera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala.