Genesis 41:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitapita zaka zimenezo, padzakhalanso zaka zisanu ndi ziŵiri za njala, ndipo zaka zonse zija za dzinthu zidzaiŵalika mu Ejipito monse. Njalayo idzaononga dziko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zochuluka zonsezo m'dziko la Ejipito; ndipo njala idzapululutsa dziko;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma zidzatsatana ndi zaka zina zisanu ndi ziwiri za njala. Chakudya chochuluka cha mu Igupto chija chidzayiwalika ndipo njalayo idzawononga dziko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zocuruka zonsezo m'dziko la Aigupto; ndipo njala idzapululutsa dziko;