Genesis 41:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Poti inu Farao mwalota kaŵiri maloto okhaokhaŵa, zikuwonetsa kuti Mulungu ndiye amene wakonza zimenezi, ndipo azichitadi posachedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo lotolo linabwezedwa kawiri kwa Farao, chifukwa chinthu chili chokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kuchichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza kuti malotowa aperekedwa kwa inu Mfumu kawiri, ndiye kuti Mulungu watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi posachedwapa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo lotolo linabwezedwa kawiri kwa Farao, cifukwa cinthu ciri cokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kucicita.