Genesis 41:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musankhenso anthu akuluakulu m'dziko lonse lino, ndipo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse za zokolola, azichiika padera pa zaka zisanu ndi ziŵiri za chakudya chochuluka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Farao achite chotere, alembe woyang'anira dziko wosonkhetsa limodzi la magawo asanu la dziko la Ejipito m'zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka dzinthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asankhenso akuluakulu a mʼdziko lino. Iwowa azitenga ndi kuyika padera limodzi la magawo asanu aliwonse a zokolola za mʼdziko muno mu zaka zonse zisanu ndi ziwiri za chakudya chochuluka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Farao acite cotere, alembe woyang'anira dziko wosonkhetsa limodzi la magawo asanu la dziko la Aigupto m'zaka zisanu ndi ziwiri zakucuruka dzinthu.