Genesis 41:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamkweza pa galeta lake lachiŵiri laufumu, ndipo alonda ake a Farao adayamba kufuula patsogolo pa galetalo kuti, “Mgwadireni.” Motero Yosefe adalandira ulamuliro, ndipo adakhala nduna yaikulu ya dziko lonse la Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anamkweza iye m'galeta wake wachiwiri amene anali naye: ndipo anafuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anamukweza Yosefe pa galeta ngati wachiwiri pa ulamuliro. Ndipo anthu anafuwula pamaso pake nati, “Mʼgwadireni!” Motero anakhala nduna yayikulu ya dziko lonse la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo anamkweza iye m'gareta wace waciwiri amene anali naye: ndipo anapfuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Aigupto,