Genesis 41:44 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Farao adauza Yosefe kuti, “Pali ine ndemwe Farao, iwe ukapanda kulola, palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kuchita kanthu kalikonse ngakhale kuyenda kumene m'dziko la Ejipito lonseli.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Ine ndine Farao, ndipo popanda iwe palibe munthu aliyense adzatukula dzanja lake kapena mwendo wake m'dziko lonse la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Farao anati kwa Yosefe, “Ine ndine Farao; tsono iwe ukapanda kulamula, palibe amene akhoza kuchita chilichonse ngakhale kuyenda kumene mʼdziko lonse la Igupto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Ine ndine Farao, ndipo popanda iwe palibe munthu ali yense adzatukula dzanja lace kapena mwendo wace m'dziko lonse la Aigupto.