Genesis 41:45 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Yosefe uja adamutcha Zafenati-Panea. Ndipo adampatsa mkazi dzina lake Asenati, mwana wa Potifera amene anali wansembe wa mzinda wa Oni. Choncho Yosefeyo adayendera dziko lonse la Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Farao anamutcha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anatuluka wolamulira, nayendayenda m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Farao anamupatsa Yosefe dzina lakuti Zafenati-Panea ndipo anamupatsanso Asenati mwana wa mkazi wa Potifara, wansembe wa Oni, kuti akhale mkazi wake. Choncho Yosefe anayendera dziko lonse la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Farao anamucha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anaturuka wolamulira, nayendayenda m'dziko la Aigupto.
Recommended Reading