Genesis 41:46 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene adayamba kugwirira ntchito Farao mfumu ya ku Ejipito. Adanyamuka, nayendera dziko lonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aejipito. Ndipo Yosefe anatuluka pamaso pa Farao, napitapita pa dziko lonse la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe anali ndi zaka 30 pamene amayamba ntchito kwa Farao, mfumu ya ku Igupto. Ndipo Yosefe anachoka pa maso pa Farao nayendera dziko lonse la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aigupto, Ndipo Yosefe anaturuka pamaso pa Farao, napitapita pa dziko lonse la Aigupto,