Genesis 41:48 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe adasonkhanitsa chakudya pa zaka zisanu ndi ziŵiri, pamene kunali dzinthu dzambirimbiri ku Ejipito, nadzisunga m'mizinda. Mu mzinda uliwonse ankasungamo chakudya cha ku minda yozungulira mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anasonkhanitsa chakudya chonse cha zaka zisanu ndi ziwiri chimene chinali m'dziko la Ejipito, nasunga chakudyacho m'midzi; chakudya cha m'minda, yozinga midzi yonse, anachisunga m'menemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe anasonkhanitsa zakudya zonse zokololedwa mʼzaka zisanu ndi ziwiri zija ndipo anazisunga mʼmizinda. Mu mzinda uliwonse anayikamo chakudya chimene chinalimidwa mʼminda yozungulira komweko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anasonkhanitsa cakudya conse ca zaka zisanu ndi ziwiri cimene cinali m'dziko la Aigupto, nasunga cakudyaco m'midzi; cakudya ca m'minda, yozinga midzi yonse, anacisunga m'menemo.