Genesis 41:49 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adasonkhanitsa tirigu wochuluka ngati mchenga wakunyanja. Kunali tirigu wochuluka kotero kuti adaaleka nkumuyesa komwe, popeza kuti kunali kosatheka kumuyesa tirigu yenseyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mchenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; chifukwa anali wosawerengeka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe anasunga tirigu wochuluka kwambiri ngati mchenga wa ku nyanja. Kunali tirigu wochuluka kwambiri motero kuti analeka nʼkulembera komwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mcenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; cifukwa anali wosawerengeka.