Genesis 41:51 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adati, “Mulungu wandiiŵalitsa kusauka kwanga konse kuja ndiponso banja la atate anga.” Motero mwana wake wachisamba uja adamutcha Manase.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe anamutcha dzina la woyamba Manase, chifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zovuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe anamutcha mwana wake woyamba, Manase popeza anati, “Mulungu wandiyiwalitsa zovuta zanga zija ndiponso banja la abambo anga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anamucha dzina la woyamba Manase, cifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zobvuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga.