Genesis 41:55 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Njalayo itakwanira dziko lonse la Ejipito, anthu ankalirira Farao kuti aŵapatse chakudya. Farao ankaŵauza onse kuti, “Pitani kwa Yosefe, zimene akakulamuleni, mukachite zimenezo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene dziko lonse la Ejipito linali ndi njala, anthu anafuulira Farao awapatse chakudya; ndipo Farao anati kwa Aejipito onse, Pitani kwa Yosefe: chimene iye anena kwa inu chitani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene njala ija inakwanira dziko lonse la Igupto anthu analilira Farao kuti awapatse chakudya. Koma Farao anawawuza kuti, “Pitani kwa Yosefe ndipo mukachite zimene akakuwuzeni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene dziko lonse la Aigupto linali ndi njala, anthu anapfuulira Farao awapatse cakudya; ndipo Farao anati kwa Aaigupto onse, Pitani kwa Yosefe: cimene iye anena kwa inu citani.