Genesis 41:56 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono njalayo itakwanira dziko lonse, Yosefe adatsekula nkhokwe za tirigu zija, namaŵagulitsa Aejipitowo, chifukwa inali itakula ndithu mu Ejipitomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo njala inali pa dziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene njala inafalikira dziko lonse, Yosefe anatsekula nkhokwe za zakudya namagulitsa tirigu kwa anthu a ku Igupto aja, pakuti njala inafika poyipa kwambiri mu Igupto monse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo njala inali pa dziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aaigupto: ndipo njala inakula m'dziko la Aigupto.