Genesis 41:57 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ankafika ku Ejipito kuchokera ku mbali zonse za dziko lapansi, kudzagula tirigu kwa Yosefe, chifukwa njala inali itakula koopsa konsekonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo maiko onse anafika ku Ejipito kudzagula tirigu kwa Yosefe: chifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ankabwera ku Igupto kuchokera ku mayiko ena onse kudzagula tirigu kwa Yosefe, chifukwa njala inafika poyipa kwambiri pa dziko lonse lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo maiko onse anafika ku Aigupto kudzagula tirigu kwa Yosefe: cifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi.