Genesis 42:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tumani mmodzi mwa inu kuti apite akamtenge. Ena nonse otsalanu mukhale m'ndende ndithu, mpaka mau anuŵa atsimikizike, tiwone ngati mukunena zoona. Apo ai, ndithu pali Farao, inuyo ndinu azondi basi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona zili mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tumizani mmodzi wa inu akamutenge mʼbale wanuyo ndipo ena nonsenu musungidwa mʼndende, kuti titsimikize ngati zimene mukunenazi ndi zoona. Apo ayi, pali Farao ndithu, inu ndinu akazitape!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona ziri mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu.