Genesis 42:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adayamba kuuzana kuti, “Ndithu, ife tidalakwa pamene mng'ono wathu ankatipempha kuti timchitire chifundo, koma ife osamumvera konse chifundo. Nchifukwa chake tili m'mavuto tsopano lino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo anati wina ndi mnzake, Tachimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anati kwa wina ndi mnzake, “Ndithu ife tinalakwira mʼbale wathu uja popeza kuti ngakhale tinaona kuvutika kwake ndi kumva kulira kwake pamene ankatidandaulira kuti timuchitire chifundo, koma ife sitinamvere. Nʼchifukwa chake masautso awa atigwera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo anati wina ndi mnzace, Tacimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kubvutidwa kwa mtima wace, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, cifukwa cace kubvutidwa kumene kwatifikira.