Genesis 42:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Rubeni adati, “Ine paja ndinkakuuzani kuti mnyamatuyu musamchite kanthu, inu osandimvera. Mwaonatu, tsopano tikulandira malipiro a imfa yake ija.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanena kwa inu kuti, Musachimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? Chifukwa chakenso, taonani mwazi wake ufunidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Rubeni anayankha, “Kodi sindinakuwuzeni kuti musamuchite kanthu mnyamata uja? Koma inu simunamvere! Tsopano tikulandira malipiro a magazi ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanena kwa inu kuti, Musacimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? cifukwa cacenso, taonani mwazi wace ufunidwa.