Genesis 42:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yosefe adalamula kuti matumba ao adzazidwe ndi tirigu, ndipo kuti ndalama za aliyense ziikidwe m'thumba mwake momwemo. Adalamulanso kuti aŵapatse kamba wapaulendo. Antchito a Yosefe adachitadi zonsezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe analamulira kuti adzaze zotengera zao ndi tirigu, ndi kubweza ndalama zao, aliyense m'thumba mwake, ndi kuwapatsa phoso la panjira; ndipo anatero nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe analamula kuti awadzazire matumba awo ndi tirigu, awayikiremo ndalama zawo momwemo ndiponso awapatse chakudya cha panjira. Izi anawachitiradi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe analamulira kuti adzaze zotengera zao ndi tirigu, ndi kubweza ndalama zao, ali yense m'thumba mwace, ndi kuwapatsa phoso la panjira; ndipo anatero nao.