Genesis 42:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaitana abale ake naŵauza kuti, “Ha, wandibwezera ndalama zanga. Si izi zili m'thumbazi.” Pamenepo onsewo mitima yao idangoti phwii! Adachita mantha kwambiri nati, “Mulungu watichita zotani ife?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anati kwa abale ake, Wandibwezera ine ndalama zanga, taonani, zili kukamwa kwa thumba langa; ndipo mitima yao inawadera iwo, nanthunthumira, natembenukirana wina ndi mnzake kuti, Nchiyani ichi Mulungu watichitira ife?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati kwa abale akewo, “Ndalama zanga andibwezera, izi zili mʼthumba mwangamu.” Mitima yawo inachita ngati yachokamo ndipo anali ndi mantha ambiri, nati, “Ndi chiyani chimene Mulungu watichitira?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anati kwa abale ace, Wandibwezera ine ndalama zanga, taonani, ziri kukamwa kwa thumba langa; ndipo mitima yao inawadera iwo, nanthunthumira, natembenukirana wina ndi mnzace kuti, Nciani ici Mulungu waticitira ife?