Genesis 42:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo iyeyo adati, ‘Kuti ndidziŵe kuti ndinu anthu okhulupirika, mmodzi mwa inu atsale ndi ine kuno, koma ena nonsenu mutenge tirigu, mupite naye ku banja la kwanu kuli njalako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziwa kuti muli anthu oona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo nduna ija inati kwa ife, “Kuti ndidziwedi kuti ndinu anthu owona mtima muchite izi: Mmodzi mwa inu atsale ndi ine kuno, ndipo enanu mutenge chakudya ndi kubwerera kwanu kumene kuli njalako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziwa kuti muli anthu oona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani;