Genesis 42:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamasula matumba ao, aliyense adapeza kuti chikwama cha ndalama chinali momwe m'thumbamo. Ataona ndalamazo, iwowo pamodzi ndi bambo wao yemweyo adachita mantha kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lake; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene amakhuthula matumba awo a tirigu aliyense anapeza kuti kathumba kake ka ndalama kali momwemo. Ataona zimenezi, iwo pamodzi ndi abambo awo anachita mantha kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lace; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa,