Genesis 42:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Rubeni adauza atate ake kuti, “Mungathe kudzapha ana anga aŵiri, ngati Benjamini sindidzabwera naye kwa inu. Mundipatse kuti ndimsamale ndine, ndipo ndidzabwera naye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Rubeni anati kwa atate wake, kuti, Muwaphe ana anga amuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m'manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Rubeni anati kwa abambo ake, “Ngati sindidzabwera naye kwa inu, mudzaphe ana anga aamuna awiri. Muperekeni mʼmanja mwangamu ndipo ndidzamusamala ndi kubwera naye kwa inu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Rubeni anati kwa atate wace, kuti, Muwaphe ana anga amuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m'manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu.