Genesis 42:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yakobe adati, “Mwana wangayu sangapite nanu ai, paja mbale wake adamwalira, ndipo ndi yekhayu watsala. Mwina mwake angathe kuphedwa pa njira, ndipo ine m'mene ndakalambiramu, chisoni chotere chidzangonditsiriza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yakobo anati, “Mwana wanga sapita nanu kumeneko; mkulu wake anamwalira ndipo watsala yekha. Ngati choyipa chitamuchitikira pa ulendo mukupitawu, ndiye kuti ndi mmene ndakalambiramu inu mudzandipha ndi chisoni chotere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, cifukwa kuti mkuru wace wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati coipa cikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi cisoni imvi zanga kumanda.