Genesis 42:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana a Israelewo adapita ku Ejipito kukagula chakudya pamodzi ndi anthu ena onse, chifukwa chakuti ku dziko la Kanani kunali njala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana amuna a Israele anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m'dziko la Kanani munali njala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ana a Israeli aja anapita pamodzi ndi gulu la anzawo kukagula tirigu pakuti ku Kanaani kunalinso njala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana amuna a Israyeli anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m'dziko la Kanani munali njala.