Genesis 42:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono popeza kuti Yosefe anali nduna yaikulu yolamulira dziko lonse la Ejipito, ndiye amene ankagulitsa tirigu kwa anthu ochokera ku mbali zonse za dziko. Choncho abale ake a Yosefe nawonso adabwera, ndipo adamgwadira Yosefeyo, namuŵeramira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yosefe anali nduna yayikulu yolamulira dziko la Igupto, ndiye kuti analinso amene ankagulitsa tirigu kwa anthu onse. Choncho abale ake a Yosefe nawonso anabwera, ndipo anamugwadira pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ace a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.