Genesis 43:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu Mphambe akuchitireni chifundo pamaso pa munthuyo, kuti abweze mbale wanu wina uja pamodzi ndi Benjamini. Ngati ana anga onse andifera, andifera ndithu basi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu chifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mulungu Wamphamvuzonse akuchitireni chifundo pamaso pa munthuyo kuti akamulole mʼbale wanu wina uja ndi Benjamini kuti abwerere ndi inu. Kukakhala kulira, ndine wolira basi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu cifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.